Joel 3

Kuweruzidwa kwa Mitundu ya Anthu

1“Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo,
nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
2ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse
ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati.
Kumeneko ndidzawaweruza
chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli,
pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu
ndikugawa dziko langa.
3Anagawana anthu anga pochita maere
ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere;
anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo
kuti iwo amwe.
4“Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu. 5Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano. 6Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.

7“Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu. 8Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.

9Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina:
Konzekerani nkhondo!
Dzutsani ankhondo amphamvu!
Asilikali onse afike pafupi ndipo ayambe nkhondo.
10Sulani makasu anu kuti akhale malupanga
ndipo zikwanje zanu zikhale mikondo.
Munthu wofowoka anene kuti,
“Ndine wamphamvu!”
11Bwerani msanga, inu anthu a mitundu yonse kuchokera ku mbali zonse,
ndipo musonkhane kumeneko.

Tumizani ankhondo anu Yehova!

12“Mitundu ya anthu idzuke;
ipite ku Chigwa cha Yehosafati,
pakuti kumeneko Ine ndidzakhala
ndikuweruza anthu a mitundu yonse yozungulira.
13Tengani chikwakwa chodulira tirigu,
pakuti mbewu zakhwima.
Bwerani dzapondeni mphesa,
pakuti mopsinyira mphesa mwadzaza
ndipo mitsuko ikusefukira;
kuyipa kwa anthuwa nʼkwakukulu kwambiri!”

14Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu,
mʼchigwa cha chiweruzo!
Pakuti tsiku la Yehova layandikira
mʼchigwa cha chiweruzo.
15Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa,
ndipo nyenyezi sizidzawalanso.
16Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni
ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu;
dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka.
Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake,
linga la anthu a ku Israeli.

Madalitso a Anthu a Mulungu

17“Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu,
ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.
Yerusalemu adzakhala wopatulika;
alendo sadzamuthiranso nkhondo.

18“Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano,
ndipo zitunda zidzayenderera mkaka;
mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi.
Kasupe adzatumphuka mʼnyumba ya Yehova
ndipo adzathirira Chigwa cha Sitimu.
19Koma Igupto adzasanduka bwinja,
Edomu adzasanduka chipululu,
chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yuda
mʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.
20Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyaya
ndi Yerusalemu ku mibadomibado.
21Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke
ndidzakhululuka.”

Yehova amakhala mu Ziyoni!
Copyright information for NyaCCL